ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Luka 1:22 - Buku Lopatulika Koma m'mene iye anatulukamo, sanathe kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya mu Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma m'mene iye anatulukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene iye adatuluka, sadathe kulankhula nawo. Apo iwo adazindikira kuti m'Nyumbamo waona china chake m'masomphenya. Iye adalankhula nawo ndi manja okha, osathanso kunena mau. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula. |
ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.
Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Aleksandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.
Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena: