inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Luka 1:16 - Buku Lopatulika Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzatembenuza Aisraele ambiri kuti abwerere kwa Ambuye, Mulungu wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. |
inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvere iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalape pambuyo pake, kuti mumvere iye.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;