Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Levitiko 8:9 - Buku Lopatulika Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adamuveka nduŵira kumutu. Kumaso kwa nduŵirayo adaikako mphande yagolide, chizindikiro chopatulira, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anamuveka Aaroniyo nduwira kumutu ndipo patsogolo pa nduwirayo anayikapo duwa lagolide, chizindikiro chopatulika monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anachita zonse zimene Yehova analamula padzanja la Mose.
Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo.