Levitiko 7:8 - Buku Lopatulika Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. |
Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.
Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,
Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera.
Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.
Pamenepo atenthe ng'ombe yaikaziyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake.