Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
Levitiko 7:7 - Buku Lopatulika Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsembe yopepesera kupalamula njofanafana ndi nsembe yopepesera machimo, ndipo nsembe ziŵiri zonsezo zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe wochita mwambo wopepesera machimo ndiye amene nyamayo ikhale yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake. |
Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.
Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pamalo opatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.
Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense.
Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.
Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe?
Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za mu Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?