Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.
Levitiko 7:3 - Buku Lopatulika Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono apereke mafuta ake onse, mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo. |
Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.
Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.
Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake.
Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.
Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.