Levitiko 7:12 - Buku Lopatulika
akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.
Onani mutuwo
akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta.
Onani mutuwo
akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta.
Onani mutuwo
“ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta.
Onani mutuwo