Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.
Levitiko 4:8 - Buku Lopatulika Ndipo achotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo achotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mafuta onse a ng'ombe yamphongo yoperekera nsembe yopepesera machimoyo, aŵachotse pamodzi ndi mafuta okuta matumbo, ndiponso mafuta ena onse okhala pamatumbopo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake achotse mafuta onse a ngʼombe yayimuna yopepesera machimoyo: mafuta okuta zamʼkati kapena mafuta onse amʼkatimo. |
Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.
Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.
Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.
Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.
nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.
Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.