Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Levitiko 4:5 - Buku Lopatulika

Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kenaka wansembe wodzozedwayo atengeko magazi a ng'ombeyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ngʼombeyo ndi kulowa nawo mu tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo



Levitiko 4:5
8 Mawu Ofanana  

Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri.


Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;


Ndipo awazepo mwazi wina ndi chala chake kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulichotsera zodetsa za ana a Israele.


akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.


Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.


Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pa chihema chokomanako.


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.