Levitiko 3:7 - Buku Lopatulika akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akapereka nkhosa kuti ikhale nsembe, abwere nayo pamaso pa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati apereka nsembe ya mwana wankhosa, abwere naye pamaso pa Yehova. |
Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.
pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosakaniza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta;
ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi.
ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?