Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Levitiko 3:4 - Buku Lopatulika

ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apatulenso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Apatulenso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake omwe ndiponso mafuta okuta chiwindi amene achotsedwa pamodzi ndi impsyo zija.

Onani mutuwo



Levitiko 3:4
15 Mawu Ofanana  

Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha paguwa la nsembe.


Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;


Ndipo aikadzule ziwalo zake, pamodzi ndi mutu wake ndi mafuta ake; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni zili pa moto wa paguwa la nsembe.


ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni zili pa moto wa paguwa la nsembe;


ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.


ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Ndipo achotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


ndi impso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso,


ndi impso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso;


Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha paguwa la nsembe.


Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;


koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha paguwa la nsembe; monga Yehova analamula Mose.


ndi mafuta a ng'ombe; ndi a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira wamafuta, ndi chophimba matumbo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa;