Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wake, nalowa m'mzinda. Pamenepo Yowabu anadza ku Yerusalemu.
Levitiko 26:7 - Buku Lopatulika Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzapirikitsanso adani anu, ndipo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu. |
Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wake, nalowa m'mzinda. Pamenepo Yowabu anadza ku Yerusalemu.
Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha.
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.
Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.
Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.
Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.
Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.
Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.
Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.
Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.