ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse;
Levitiko 2:7 - Buku Lopatulika Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo nsembe yako ikakhala ya chopereka cha chakudya chophika pa chiwaya, chikhale ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophikidwa pa chiwaya, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. |
ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse;
Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe.
Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.