Levitiko 2:5 - Buku Lopatulika Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosakaniza ndi mafuta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosanganiza ndi mafuta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsembe yako ikakhala chakudya chophika pa chitsulo chamoto, chikhale buledi wa ufa wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati nsembe yako yachakudya ndi yophika pa chitsulo chamoto, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta. |
Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova.
akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.
Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;