Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
Levitiko 2:16 - Buku Lopatulika Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono wansembe atenthe chigawo cha mbeu zopunthapuntha zija ndi cha mafuta, ndiponso lubani wake yense, kuti ikhale nsembe yachikumbutso. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono wansembe atenthe gawo la chopereka chopunthapuntha chija kuti chikhala ufa wachikumbutso ndi cha mafuta pamodzi ndi lubani yense kuti Yehova alandire mʼmalo mwa zopereka zonse. Ichi ndi chopereka chotentha pa moto cha Yehova. |
Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi paguwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize paguwa la nsembe zichite fungo lokoma.
Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola.
Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,