nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.
Levitiko 18:3 - Buku Lopatulika Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo. |
nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza.
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye mu unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao.
Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golide, zokhala pakati pao;
Musamanena mumtima mwanu, atawapirikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Chifukwa cha chilungamo changa Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.