Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, aakulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.
Levitiko 15:3 - Buku Lopatulika Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m'thupi mwake, ngakhale chaleka m'thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m'thupi mwake, ngakhale chaleka m'thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lamulo lake lokhudza za kudziipitsa ndi zonyansa zotuluka ku maliseche a munthu nali: malisechewo akamatulutsabe mafinya, kaya aleka, munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lamulo lokhudza kudziyipitsira ndi zotuluka ku maliseche a munthu nali: Malisechewo akamatulukabe mafinya, kaya aleka, munthuyo adzakhala wodetsedwa: |
Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, aakulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.
Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya abulu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.
Nenani nao ana a Israele, nimuti nao, Pamene mwamuna aliyense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwake, akhale wodetsedwa, chifukwa cha kukha kwake.
Kama aliyense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi chinthu chilichonse achikhalira chili chodetsedwa.