Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa;
Levitiko 11:9 - Buku Lopatulika Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Zamoyo zam'madzi zimene mutha kudya ndi izi: zonse zam'madzi zimene zili ndi zilimba ndi mamba, mungathe kudya, ngakhale zikhale zam'nyanja kapena zam'mitsinje. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi a mʼnyanja ndi a mʼmitsinje mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. |
Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa;
ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.
Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.