Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.
Levitiko 11:4 - Buku Lopatulika Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, angakhale abzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Koma pali nyama zina zimene zimabzikula kokha kapena ndi zogawikana zipondero zimene simukuyenera kudya. Nyama zimenezi ndi ngamira, ngakhale imabzikula ilibe zipondero zogawikana. Choncho ndi yodetsedwa, musadye. |
Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.
Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.
Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.