Levitiko 11:3 - Buku Lopatulika Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ‘Nyama zonse zokhala ndi ziboda zogaŵikana, ndi zobzikula, angathe kudya zimenezo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya. |
Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.
Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa.
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.
Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa.
Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.
Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,
Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.
ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.