Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
Levitiko 11:2 - Buku Lopatulika Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Awuze Aisraeli kuti, ‘Nyama zomwe mukhoza kudya mwa nyama zonse za dziko lapansi ndi izi: |
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse.
Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;
Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kutumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi:
Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake;
Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya.
Chakudya chilichonse chokhala m'mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m'chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa.
Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, ingakhale ibzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa.
Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya.
si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.