Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.
Levitiko 11:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anayankhula ndi Mose ndi Aaroni kuti, |
Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.
Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili padziko lapansi.
Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa.
Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.