Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Levitiko 10:7 - Buku Lopatulika Ndipo musatuluka pakhomo pa chihema chokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anachita monga mwa mau a Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo musatuluka pakhomo pa chihema chokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anachita monga mwa mau a Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano kuti mungafe, chifukwa mudadzozedwa ndi mafuta a Chauta.” Iwo adachita monga momwe Mose adanenera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano, mungafe, chifukwa munadzozedwa ndi mafuta a Yehova kukhala ansembe.” Choncho iwo anachita monga Mose ananenera. |
Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.
Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.
Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.
Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.