Levitiko 1:6 - Buku Lopatulika Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo asende nyamayo ndi kuidula nthulinthuli. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthuyo asende nsembe yopserezayo ndi kuyidula nthulinthuli. |
Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.
Ndi zichiri zangowe, chikhato m'litali mwake, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.
Ndipo ana a Aroni wansembeyo asonkhe moto paguwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;
Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense.