Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere paguwa la nsembelo.
Levitiko 1:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'chihema chokomanako Iye, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'chihema chokomanako Iye, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Chauta anali m'chihema chamsonkhano adaitana Mose, namuuza kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero 26 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati, |
Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere paguwa la nsembelo.
Ndi kuwerenga kwake kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi anaankhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova.
Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.
Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano.
Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
chimene Yehova analamulira Mose m'phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israele abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m'chipululu cha Sinai.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.
Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.
Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;