Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
Hoseya 9:5 - Buku Lopatulika Mudzachitanji tsiku la misonkhano yoikika, ndi tsiku la chikondwerero cha Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mudzachitanji tsiku la masonkhano oikika, ndi tsiku la chikondwerero cha Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi pa tsiku la chikondwerero, tsiku lolemekeza Chauta, anthuwo adzachitapo chiyani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika; pa masiku a zikondwerero za Yehova? |
Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?
Ndidzaleketsanso kusekerera kwake konse, zikondwerero zake, pokhala mwezi pake, ndi masabata ake, ndi misonkhano yake yonse yoikika.
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.