Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Hoseya 8:4 - Buku Lopatulika Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Amadzilongera mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amadziikira atsogoleri popanda chilolezo changa. Adzipangira mafano asiliva ndi agolide, koma adziwononga nawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo. |
Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga padziko lapansi.
Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira.
Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?
Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni.
Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.
Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.
Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.
Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;
ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama.
koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?