Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Hoseya 8:12 - Buku Lopatulika Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidaŵapatsa malamulo ambiri olembedwa, koma saŵasamala. Amaŵayesa achilendo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga, koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo. |
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.
Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.
Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.