chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.
Hoseya 8:11 - Buku Lopatulika Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Aefuremu adachulukitsa maguwa ansembe ochotserapo machimo, koma maguwawo asanduka malo ochimwirapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo, maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo. |
chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.
Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.
Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.
Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova.
Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.