Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Hoseya 7:10 - Buku Lopatulika Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele kunyada kwao komwe kukuŵatsutsa. Koma pa zonsezi sakubwerera kwa Chauta Mulungu wao, sakumfunafuna konse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa, koma pa zonsezi iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake kapena kumufunafuna. |
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.
Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale, koma utsiru wake sudzamchoka.
Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.
Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.
Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.
Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.