Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.
Hoseya 5:6 - Buku Lopatulika Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amapereka nsembe zankhosa ndi zang'ombe pofunafuna Chauta, koma samupeza, waŵachokera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo kukapereka nsembe kwa Yehova, iwo sadzamupeza; Iye wawachokera. |
Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.
Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.
Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;
Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.
Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao.
Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.
Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.
Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau aakulu, koma sindidzawamvera Ine.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.
Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.
Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.