Hoseya 5:12 - Buku Lopatulika Ndipo ndikhala kwa Efuremu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati chivundi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndikhala kwa Efuremu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati chivundi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake ndidzaononga Efuremu, monga momwe njenjete zimaonongera nsalu, ndidzakhala ngati chilonda choola pa anthu a ku Yuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu, ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda. |
Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? Taonani, iwo onse adzatha ngati chovala, njenjete zidzawadya.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse.