Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
Hoseya 4:4 - Buku Lopatulika Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti, “Wina aliyense asatsutsepo kanthu, wina aliyense asaimbe mnzake mlandu, pakuti mlandu uli pakati pa Ine ndi inu ansembe onyenganu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Koma wina asapeze mnzake chifukwa, wina aliyense asayimbe mlandu mnzake, pakuti anthu ako ali ngati anthu amene amayimba mlandu wansembe. |
Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.
ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.
Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.