Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.
Hoseya 4:18 - Buku Lopatulika Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amati akamwa kwambiri, amangochita zigololo. Amakonda zamanyazi kupambana ulemu wao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha, amapitiriza kuchita zachiwerewere; atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi. |
Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto.
Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo.
Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama.
Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?
Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake.
Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.
Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.
Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.
Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.
Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.