Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
Hoseya 3:2 - Buku Lopatulika M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero ndidamkwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iŵiri ya barele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. |
Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.
Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.
Chifukwa kuti munda wampesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi.
Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.
ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe.
Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.
Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.
Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti.