Hoseya 2:6 - Buku Lopatulika Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Nchifukwa chake njira yake ndidzaitseka ndi minga. Ndidzamuzinga ndi khoma, kuti asayendenso m'njira zake zakale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga; ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira. |
Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;
Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.
Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.