Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Hoseya 2:12 - Buku Lopatulika

Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama za kuthengo zidzaidya.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndidzaononga mitengo yake yamphesa ndi yankhuyu imene ankanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo malipiro anga amene zibwenzi zanga zidandipatsa.’ Ndidzaisandutsa malunje, ndipo zilombo zizidzadya kumeneko.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu, imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake. Ndidzayisandutsa chithukuluzi, ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.

Onani mutuwo



Hoseya 2:12
14 Mawu Ofanana  

Munapasuliranji maphambo ake, kotero kuti onse akupita m'njira atcherako?


Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?


Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wampesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi;


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.


Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.


Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.


Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.


Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.