Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?
Hoseya 13:4 - Buku Lopatulika Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti “Ine ndakhala Chauta Mulungu wako kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito. Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha, Mpulumutsi wako ndine ndekha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mu Igupto. Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha, palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine. |
Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?
Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.
Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi padzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.
Ndipo ndidzampatsa minda yake yampesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito.
Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.