Cholakwa changa chaikidwa m'thumba lokhomedwa chizindikiro; ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.
Hoseya 13:12 - Buku Lopatulika Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kuipa kwa anthu a ku Efuremu kwalembedwa m'buku, buku lake la machimo ao ndalisunga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa, machimo ake alembedwa mʼbuku. |
Cholakwa changa chaikidwa m'thumba lokhomedwa chizindikiro; ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.
Mukuti, Mulungu asungira ana ake a munthu choipa chake, ambwezere munthuyo kuti achidziwe.
Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.
Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;