Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
Hoseya 11:9 - Buku Lopatulika Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mzinda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse, sindidzamuwononganso Efuremu, pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu. Ine, Woyera uja, ndili nawe, ndipo sindidzabwera kudzakuwononga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa, kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu. Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu, Woyerayo pakati panu. Sindidzabwera mwaukali. |
Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.
Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.
Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse.
Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.
Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.
Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.
Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;
Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.