Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Hoseya 1:9 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamenepo Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Si-anthu-anga’, pakuti inu Aisraele sindinunso anthu anga, ndipo Ine sindinenso Mulungu wanu.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.

Onani mutuwo



Hoseya 1:9
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.


Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.


Ataleka tsono kuyamwitsa Wosachitidwa-chifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.


Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.