Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Hoseya 1:3 - Buku Lopatulika Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Hoseya adapita, nakakwatira mkazi, dzina lake Gomeri, mwana wa Dibulaimu. Mkaziyo adatenga pathupi, namubalira mwana wamwamuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. |
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng'ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.