Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.
Hagai 1:3 - Buku Lopatulika Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti, |
Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.
Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti,
Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.
Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zochingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka?
Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,