Genesis 9:22 - Buku Lopatulika Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja. |
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao!
Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.