Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.
Genesis 9:21 - Buku Lopatulika namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche. |
Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.
Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.
njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro.
ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.