Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Genesis 9:19 - Buku Lopatulika Amenewa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Nowa atatu ameneŵa ndiwo makolo a anthu a pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi. |
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.