Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;
Genesis 9:17 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimenechi ndi chizindikiro cha chipangano chimene ndachita ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.” |
Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo padziko lapansi.
Ndi ana aamuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti. Hamu ndiye atate wake wa Kanani.
Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;