Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu.
Genesis 8:6 - Buku Lopatulika Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku makumi anai, Nowa adatsekula zenera, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo |
Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu.
Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.
ndipo anatulutsa khwangwala, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi padziko lapansi.
Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse.