Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi.
Genesis 8:17 - Buku Lopatulika Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi; kuti ziswane pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwezo, mbalame, nyama ndi zokwaŵa, kuti ziswane ndi kubalalika pa dziko lonse lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.” |
Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi.
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Tulukamoni m'chingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.