Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu.
Genesis 7:20 - Buku Lopatulika Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adakwererakwerera ndithu mpaka kubzola nsonga za mapiriwo mamita asanu ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri. |
Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu.
Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pathambo lonse.
Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.
Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.